Madalitso a Mulungu pa moyo wanga amabwera nthawi zonse mokwanira ndipo amafika panthawi yake, sakhala mochedwa. Mulungu amadziwa nthawi yoyenera yotumizira madalitso amene mumapempha m’pemphero.
Tizunguliridwa ndi madalitso okongola a Mulungu, tili ndi thanzi, tili ndi pogona, tili ndi chakudya, tili ndi thanzi la maganizo, tili ndi anthu amene amatikonda ndipo koposa zonse tili ndi Mulungu m’miyoyo yathu, timasangalala ndi mphatso yabwino ya chipulumutso, amenewa ndi madalitso amene nthawi zina sitimazindikira, koma amene anthu ambiri akusowa, ndipo tiyenera kuyamikira zinthu zimenezi, ndi kusangalala chifukwa chifundo cha Mulungu chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse.
Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu zonse mogwirizana ndi chuma chake cha ulemerero mwa Khristu Yesu (Afilipi 4:19). Mulungu amalankhula m’mawu ake kuti madalitso ochokera kwa Iye ndi amene amalimbitsa ndipo saonjezera chisoni, Mulungu amadziwa zimene tikufuna ndipo amasamalira ife.
Tikhale oleza mtima kuti madalitso ake adzafika pamene simukuyembekezera. Lambirani Ambuye Mulungu wanu, ndipo adzadalitsa chakudya chanu ndi madzi anu. Ine ndidzachotsa matenda onse pakati panu (Ekisodo 23:25). Khalani ndi moyo womvera Mulungu ndipo madalitso adzabwera nawo.
Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.
Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;
Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.
Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.
Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakutula ndi mwana wochititsa manyazi.
Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.
Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita; Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu. Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake. Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo. ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.
Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Yehova analumbira pa dzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito; koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.
Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.
ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.
Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.
koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako. azikhala nawe ngati wolipidwa ntchito, ngati mlendo wako; akutumikire kufikira chaka choliza lipenga. Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake. Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo. Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako. Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo aamuna ndi aakazi. Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anuanu. Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m'mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza. Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera chuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa fuko la banja la mlendo; atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole; kapena mbale wa atate wake, kapena mwana wa mbale wa atate wake amuombole, kapena mbale wake aliyense wa banja lake amuombole; kapena akalemera chuma yekha adziombole yekha. Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.
Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe. Zipatso zoyamba zonse zili m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.
ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.
Mutasenga dzinthu zanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'ntchito zonse za manja anu.
Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.
Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.
Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu.
Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa ambuyake.
Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.
Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi, wofuula ndi mau akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.
Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula. Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.
tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.
Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.
Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.
Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.
Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.
Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.
Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.
Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.
Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye.
Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
Ndiponso udzalima minda ya mphesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.
Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.
ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.
Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake; koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi? Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu. Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.
Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.
Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba. Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.
Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.
Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama za kuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako wa azitona.
Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,
Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.
Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe. Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.
Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa m'chitunda cha zipatso zambiri; Chifukwa kuti munda wamphesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi. Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake. Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi. Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo. Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wotchuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa; koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo. Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo. Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zachabe, ndi tchimo ngati ndi chingwe cha galeta; amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe! ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.
Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mudzi umodzi mvula, osavumbitsira mudzi wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.
Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.
Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba.
Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.
Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako amuna undipatse Ine.
Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.
Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili.
Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza;
Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.
Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo. Pakuti m'menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso. Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao.
Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao.
mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo;
Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;
pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiika pansi, mututa chimene simunachifesa. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiika, ndi wotuta chimene sindinachifesa; ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake?
Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.
Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.
Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yamphesa ndi kudya chipatso chake.
Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m'dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.
Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.
Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga.
Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.
Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa. Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka. Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja, nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake. Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi? Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino? Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.
Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? Kodi amachocholabe, ndi kuswa zibuma za nthaka? Atakonza thyathyathya pamwamba pake, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ake osankhika, ndi mchewere m'maliremo?
Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka m'Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.
Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa. Koma chaka chachinai zipatso zake zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova. Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zolemeza. Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao.