Atate wathu wakumwamba watilangiza kuti tizipemphera nthawi zonse. Ndi m’pemphero momwe timayanjana ndi Mulungu wathu. Pemphero ndi njira yolankhulirana ndi Mulungu. Ndi m’pemphero momwe timaperekera mapempho athu onse pamapazi a Mlengi wathu. Ndi komwe timapita zinthu zikavuta, tili ndi nkhawa, kapena titakhala achisoni.
Mulungu amadziwa kale zosowa zathu, ndipo ankadziwa miyoyo yathu tisanabadwe. Koma amafuna kuti tizilankhula naye, kuti timufunefune. Mukapemphera, mumayamba kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Mumapanga ubale wolimba naye. Pemphero ndi chida champhamvu kwa ife okhulupirira Yesu. Ndi chida chodzitetezera pa nkhondo iliyonse. Ndi m’pemphero momwe mumapezera chipambano pa chilichonse.
Mphamvu ya pemphero sichokera kwa inu, koma kwa Yesu. Iye ndiye amayankha mapemphero ndi kuchititsa zinthu zomwe sizingatheke kwa anthu. Mukapemphera ndi mtima wonse, mumapeza chitonthozo, mtendere, ndi chikondi cha Atate. Yandikirani kwa Mulungu ndi mtima wodzichepetsa ndi wachisoni, ndipo sadzakukanani. (Aefeso 6:18)
Pemphani mwa Mzimu nthawi zonse, ndi mapempho osiyanasiyana. Khalani maso, ndipo pempherani nthawi zonse chifukwa cha oyera mtima onse. Mukapemphera, yambani ndi kuyamika Mulungu. Osangopereka mapempho anu okha, komanso khalani chete pamaso pake. (Atesalonika 1 5:16-18) Khalani okondwa nthawi zonse, pempherani nthawi zonse, ndipo yamikani Mulungu pa chilichonse, pakuti ichi ndi chifuniro chake kwa inu mwa Khristu Yesu.
Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.
Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye;
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?
Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m'mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Yehova wa moyo wanga.
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,
Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.
Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.
Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israele, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululukire.
nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,
Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera,
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,
Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.
Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
Koma mucheukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwake kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;
ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?
Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse chomkomera chonse, ndi ntchito ya chikhulupiriro mumphamvu;
Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.
koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.
Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu.
Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva m'Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.
Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zolakika, zimene suzidziwa.
Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.
Yehova, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Ndimkonda, popeza Yehova amamva mau anga ndi kupemba kwanga. Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ndinazunzika kwambiri. Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza. Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira? Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova. Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse. M'mabwalo a nyumba ya Yehova, pakati pa inu, Yerusalemu. Aleluya. Popeza amanditcherera khutu lake, chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,
amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.
Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;
Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa. Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero. Wolemekezeka Mulungu, amene sanandipatutsire ine pemphero langa, kapena chifundo chake.
Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwao.
ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.
Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!