M'Baibulo muli mavesi ambiri amene amandilimbikitsa kukhala wachifundo. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 19:1717 limati: “Wochitira chifundo munthu wosauka akukongola Yehova, ndipo adzam’bwezera zabwino zake.” Apa tikumva kuti kuchitira chifundo osauka sikungokhala kuchita zabwino kwa anzathu okha, komanso njira yolemekezera Mulungu.
Kufanana ndi Yesu, m'Chipangano Chatsopano mu Mateyu 14:1414, timva kuti Yesu ataona khamu la anthu lomutsatira, “anamvera chifundo, nachiritsa odwala awo.” Izi zikusonyeza kuti chifundo chimagwirizana ndi kufuna kuthandiza ndi kuchiritsa ena, monga momwe Yesu anachitira ali padziko lapansi.
Ndikufuna kuti mumvetse kuti chifundo ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wa munthu. Mawu a Mulungu amatiphunzitsa kukhala achifundo kwa anansi athu, kuwapatsa chitonthozo, chithandizo ndi kuwakhululukira. Tikamachita chifundo, sitikungotsatira malamulo a m’Baibulo okha, komanso tikumanga ubale wolimba ndi kupanga dziko labwino kwa tonse.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka, chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.
Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?
Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.
Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.
Ndipo Iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo.
Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?
Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo, nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.
Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.
Iye adzadyetsa zoweta chake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa pachepa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao.
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.
Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
Koma pamene anawalamulira iwo achoke m'bwalo la akulu, ananena wina ndi mnzake,
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.
kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?
Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha m'Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo; angaleke kuopa Wamphamvuyonse.
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;
Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.
Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda. M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu; Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona. Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.
Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.
Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.
Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.
Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga.
Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.
Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.
Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja; Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake. kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu. Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),
Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse. Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.
Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu. Ndipo anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.
Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse. Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi. Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.
Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako. Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.
Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;