Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


Mavesi a m’Baibulo onena za Mzimu Woyera

Mavesi a m’Baibulo onena za Mzimu Woyera


Yohane 14:26

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:25

Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:3-4

Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake; iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwa m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaona chivunde. Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva. Pakuti Davide sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako. Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika. Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale? Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:14

Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:2

Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:13

Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 3:17

Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:5

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:27

Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26

Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:13-14

Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani. Iyeyo adzalemekeza Ine; chifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:19

Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:32

Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11

musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15

Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:16

Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:21

chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:17

Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:15-17

Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga. Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-17

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:10

Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:6

Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:3

ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26-27

Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:11

Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:17

kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:1

Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 4:6

Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 143:10

Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:24

Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:13

m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:4

Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:13

Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:24

Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:9

Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:13-14

Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:38-39

Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake. Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44-47

Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha, Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:22

amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:11

Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:12-13

Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu. Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:2

ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:5-6

Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:17-18

Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:4

pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18

Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:17

ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:15-17

amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera: pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:14

Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:12

Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15-16

Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:18

kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:2

Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:8

Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa