Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


MAVESI A MPHAMVU

MAVESI A MPHAMVU

Ndimakondwa kwambiri kudziwa kuti ngakhale mavuto amene tingakumane nawo pa moyo wathu, tili ndi mphamvu ya Mulungu mwa ife. Ana a Mulungu sitimakhala tokha pa vuto lililonse, Mulungu nthawi zonse amakhala nafe. Ambuye amatitsogolera, akumenyera nkhondo zanu ndi kukudzazitsani ndi mphamvu Yake kuti mupambane pa vuto limene mukukumanalo.

Mu 2 Akorinto 12:9-10, Mulungu akutiuza kuti chisomo Chake chikwanira chifukwa mphamvu Yake imaonekera bwino mu kufooka kwathu. Ndi chinthu chokondweretsa kudziwa kuti pakati pa mavuto amene mukulimbana nawo, kufooka kwanu, Mulungu ali pomwepo akutsimikizira mphamvu Yake mwa inu.

Mulungu amatipatsa mphamvu Yake. Mu Luka 24:49, akuti, “Ndipo onani, Ine ndikutumizirani lonjezo la Atate wanga; koma inu khalani mumzinda wa Yerusalemu kufikira mutavala mphamvu yochokera kumwamba.”

Tili ndi Mulungu Wamphamvuyonse, palibe chomwe chingamulephere, angathe kuchita chilichonse. Mukhulupirire Iye ndipo adzagwira ntchito m'moyo wanu.




Machitidwe a Atumwi 2:1-2

Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi.Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:3-4

Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha.Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:31

Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:26

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:22-24

Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 11:15

Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:25-28

Pakuti Davide anena za Iye, Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse; chifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo.Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,munandidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:15

kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:37-39

Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:33

Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:2

Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:4-5

ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26

Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:4

Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:5

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:3

Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:49

Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:5

pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:16-17

Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse,ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:41

Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:32

Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:9-11

Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo.Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:17

Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:18

ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:19-21

Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pa dziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera.Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:28-29

Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:30

Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:3

Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:43

Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:19-20

Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44-46

Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 11:15-16

Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:1-6

Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane.Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26-27

Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:12

Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:13-14

Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:18

kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:19

Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:27

kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:8

Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:4

pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:15-17

Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena,Ichi ndi chipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;ndipo machimo ao ndi masaweruziko ao sindidzawakumbukiranso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:20

Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:24

Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:8

Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:46

Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:16

Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:7

Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:21-22

Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:5

Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:14

Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:25

Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:22

chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:1

Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:15

Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:13

m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:9-11

Ndipo m'mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao;amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:14

Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:47

nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6-8

Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:16

Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:14-17

Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:45

Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:47

Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:2

ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:11

Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:15

Atumiza lamulo lake kudziko lapansi; mau ake athamanga liwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:2

Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:21

Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:18

Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17-18

Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:13

Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:37-39

Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:13

Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:1

Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:42

Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:19

Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:15-17

amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:17

Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 11:24

chifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidaonjezeka kwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:52

Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:22

nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 15:8

Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:7

pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:23

koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15

Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:27

ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:10-12

Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:1

Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:9-10

pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4

Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:12-13

Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:10

Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:16

Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:11

Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:15-21

Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku;komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yowele,Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pa dziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera.Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:33

Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:55

Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:18

Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:19

Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:22

amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:16-17

Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:3

Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:19

Musazime Mzimuyo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:1

Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:25-26

Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1-2

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:135

Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; ndipo mundiphunzitse malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:1-5

Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga;kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira;ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire;ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:11

Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:2

Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37-38

Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18

Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:32-33

Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye.Ndipo sindinamdziwa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4-6

Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza,koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:3-4

Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha;mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili pa dziko lapansi m'chilakolako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:20-21

Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.Sindinakulemberani chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:19

Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:4

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kachisi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:6

Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Zikomo Ambuye, ndinu wochiritsa wanga, wopereka wanga, ndi mlonda wanga. Ndinu amene mumalungamira nkhondo zanga, ndi kunditsogolera kuchokera ku ulemerero kupita ku ulemerero. M'dzina lamphamvu la Yesu, ndikubwera kwa Inu, ndikukuthokozani chifukwa pemphero ndi chida champhamvu kwambiri chothetsera mavuto aliwonse, ndiye chinsinsi chotsegulira zitseko zonse. Ambuye, mwatiitana kukhala mchere wa dziko lapansi ndi kuunika kwa dziko, kuti tionetse ulemerero wanu ndi mphamvu zanu kulikonse kumene tingapite. Mu mau anu mukuti, "Ndipo ndakuyika iwe kuti ndionetse mphamvu yanga mwa iwe, ndi kuti dzina langa lidzalalikidwe pa dziko lonse lapansi." Ambuye Yesu, ndithandizeni kukhala wokhazikika ndi kupemphera nthawi zonse ndi pemphero lililonse ndi pembedzero mwa Mzimu, mundiphunzitse kukhala maso ndi kudzuka ngati wopempherera, ndikuteteza banja langa, mtundu wanga, ndi abale anga m'chikhulupiriro. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa