Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


NDIME ZA UCHIMO

NDIME ZA UCHIMO

Tanthauzo lenileni la mawu oti uchimo ndi “kuphonya pafupi ndi cholinga.” Zikutanthauza kuti tikapalamula, sitikwaniritsa kapena timalakwitsa zomwe tikayenera kuchita. Uchimo umatipatula ndi Mulungu, koma tili ndi magazi ake amtengo wapatali omwe amatitsuka ku uchimo wonse, kudzera m’kutembenuka mtima.

Lingaliro la uchimo m’Baibulo likutanthauza kuswa lamulo la Mulungu. Mkristu weniweni safuna kuchimwa, akachimwa, zimamutsutsana ndi mtima wake, chifukwa cha uchimo umene tonse tiri nawo. Machimo onse amakhululukidwa, mwa chisomo cha Mulungu, chifukwa cha ntchito ya Khristu.

Koma, onamizira kukhala Akristu, amakhala ndi uchimo wobisika, chifukwa amapitirizabe monga momwe analiri asanakhale Akristu, koma okhala ngati oyera pamwamba pake; kwenikweni, akadali ochimwa. “Ngati tinena kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo choonadi sichiri mwa ife. Koma ngati tivomereza machimo athu, Iye ali wokhulupirika ndi wolungama kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutiyeretse ku zoipa zonse. Ngati tinena kuti sitinachimwe, timuyesa Iye wabodza, ndipo mawu ake sali mwa ife.” (1 Yohane 1:8-10)

Kukhala ndi uchimo sikutanthauza kuchita uchimo kapena kukhala m’uchimo. Apa Lemba likutilengeza zomwe tonse tikudziwa, kuti tikadali ndi zotsatira za uchimo, ndipo timachimwa. Palibe amene alibe uchimo. Mphatso ya Mulungu kwa ife ndi chisomo chake. Ndipo ichi, chowululidwa kudzera mwa Yesu, ndi champhamvu kwambiri kuposa uchimo.

Yesu, Mulungu wodzitukumula, anabwera kudziko lapansi kuti tonse tipeze mwayi wokhululukidwa machimo athu. Iye anavomera kufera pamtanda ndi kunyamula machimo athu kuti kudzera mu nsembe yake tipeze moyo wosatha.




1 Yohane 5:21

Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:23

Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:3-5

Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko. Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 13:4

Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:7-9

Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate wao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:14-15

Musamatsata milungu ina, milungu ina ya mitundu ya anthu akuzinga inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:39

Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi pa dziko lapansi; palibe wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:4-8

Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao. Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 13:4

Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:15-18

Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu. Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya. Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:18-20

Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani? Fano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golide analikuta ndi golide, naliyengera maunyolo asiliva. Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse. Wosowa nsembe yoteroyo asankha mtengo umene sungavunde, iye adzisankhira yekha munthu mmisiri waluso, akonze fano losema, limene silisunthika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 24:15

Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:3-5

Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa. Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike. Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 24:23

Ndipo tsopano, chotsani milungu yachilendo ili pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:3-5

Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi? Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji; kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:7

Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:9

Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8-9

Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao; koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 26:1

Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 2:8

Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:4

Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 32:1-4

Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu. Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba? Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu. Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse. Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake. Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe. Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo. Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono. Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa olakika, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe. Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri. Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine. Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere? Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba choipa. Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. Ndipo ndinanena nao, Aliyense ali naye golide amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m'moto, ndimo anatulukamo mwanawang'ombe uyu. Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao, Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye. Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake. Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu. Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino. Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu. Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m'buku lanu limene munalembera, Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa. Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndipo Yehova anakantha anthu, chifukwa anapanga mwanawang'ombe amene Aroni anapanga. Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:4

Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:5

Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 11:12

Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzafuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:14

Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:15

Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:13

Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:20

Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:21-23

chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa; nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:20

Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:16-31

Pamene Paulo analandira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano. Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao. Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa. Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe? Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira, Pakuti ufika nazo kumakutu athu zachilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani? (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.) Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa. Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu. Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja; satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao; kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake. Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu. natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu. Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima; chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 23:13

Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:6

Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama, koma ndikhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 11:2

Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:8

Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza ntchito ya manja aoao, imene zala zaozao zinaipanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:23

nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 5:13

ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:36-39

Ndipo anatumikira mafano ao, amene anawakhalira msampha: Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda, nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo. Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Habakuku 2:18

Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 18:21

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:16

Pamene Paulo analandira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 17:15-17

Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa. Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala. Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:13

Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m'phiri langa lopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:5-6

Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako kunjira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga kunjira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pake. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:17-18

Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m'menemo. Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:4

Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:17

Usadzipangire milungu yoyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25-26

Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu. Musamalowa nacho chonyansachi m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:2

Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:29

Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:6-7

Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu. Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazikitsire Ine anthu akale? Milunguyo iwadziwitse zomwe zilinkudza, ndi za m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:14

Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya mwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:8

Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 8:4-6

Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi. Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri; koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:1-2

Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama. ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse; ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso. Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutali ndi chilungamo; ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m'Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga. Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 2:8-9

Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:25

amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:41-43

Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao. Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu? Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 33:7-9

Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse; ndipo sindidzasunthanso phazi la Israele kudziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kuchita zonse ndawalamulira, chilamulo chonse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose. Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:7

Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 9:21

Ndipo ndinatenga tchimo lanu, mwanawang'ombe mudampangayo, ndi mumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati fumbi; ndipo ndinataya fumbi lake m'mtsinje wotsika m'phirimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:22

Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:7

Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera m'Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:24

Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:37

Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:30-31

dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? Ndichite momwemo inenso. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:38

nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:10

Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:19

Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali ina pamoto, inde ndaochanso mkate pamakala pake, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndichipange chotsala chake, chikhale chonyansa? Ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:15

nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 34:33

Yosiya nachotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka m'Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:39

Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:12

Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 1:16

Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:8

Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:1

Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:20-22

Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda. Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda. Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:9

Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:4

Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:16

Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:13

Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:8

Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:3-4

Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda. Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8

Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:1-2

Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo. Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wa makamumakamu, ndiye Mfumu ya ulemerero. Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:18

Ndimo mafano adzapita psiti.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:19

Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:21

Munadzudzula odzikuza otembereredwa, iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 16:31-33

Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira. Nammangira Baala guwa la nsembe m'nyumba ya Baala anaimanga m'Samariya. Ahabu anapanganso chifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israele adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:1

Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 44:17-19

Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa. Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi chaola. Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:5

Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 28:1-3

Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake, Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi milandu yopalamula kwa Yehova Mulungu wanu? Mundimvere tsono, bwezani andende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu. Pamenepo akulu ena a ana a Efuremu, Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo, nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutipalamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa machimo athu ndi zopalamula zathu; pakuti tapalamula kwakukulu, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israele. Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga msonkhano wonse. Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya. Nthawi yomweyo mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asiriya amthandize. Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende. Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi milaga yake, ndi Timna ndi milaga yake, ndi Gimizo ndi milaga yake; nakhala iwo komweko. Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri. koma anayenda m'njira za mafumu a Israele, napangiranso Abaala mafano oyenga. Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa. Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo. Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo. Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse. Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngodya zilizonse za Yerusalemu. Ndi m'midzi iliyonse ya Yuda anamanga misanje ya kufukizira milungu ina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ake. Machitidwe ena tsono, ndi njira zake zonse, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele. Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:28-32

Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera; anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi, akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo; amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:9

Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:14

pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:28

Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pochita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:11

Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:10-11

Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo. Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m'dera lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:15-19

Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake. Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kuchitika. Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo. Unatenganso zovala zako za nsalu yopikapika, ndi kuwaveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi chofukiza changa pamaso pao. Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uchi, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zichite fungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:14

monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:15

kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 17:8

Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wachilungamo ndi wokhulupirika, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu! Ambuye Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha nsembe yanu pa mtanda, kutenga malo anga ndi kulipira mtengo umene sindikanatha kulipira. Zikomo potsegula njira yatsopano yotchedwa chipulumutso kwa anthu onse. Ndikukupemphani mundithandize ndi kundimasula ku chilichonse chomwe chimandimanga ku uchimo. Mawu anu amati: "Pakuti malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye wathu." Ambuye Yesu, limbitsani ndi kukonzanso munthu wanga wamkati, ndithandizeni kuvuala munthu wakale amene ali ndi zilakolako zonyenga ndi kusapatsa uchimo malo m'moyo wanga, koma kukana chilakolako chilichonse ndi chilichonse chomwe chimandipangitsa kuchimwa. Zikomo Yesu, chifukwa cha nsembe yanu yangwiro munalipira ngongole yanga, munandiwombola, munandipulumutsa ndipo tsopano ndine womasuka ku chiweruzo chilichonse. Ambuye, ndithandizeni kupambana ndi kutseka chitseko chilichonse cha uchimo kuti ndidane ndi kuchotsa m'moyo wanga zizolowezi zoipa, dama, zolaula, bodza, chilakolako, umbombo, chigololo ndi chonyansa chilichonse. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa