Ukwati ndi chinthu chopangidwa ndi Mulungu, kuti munthu asakhale yekha. Ndi ubale wapadera komanso wodabwitsa umene umafuna kudzipereka ndi kupirira. Monga ana a Mulungu tiyenera kusonyeza chikondi chake ndipo ukwati umatipatsa mwayi tsiku ndi tsiku wochisonyeza.
Tili ndi mavesi ambiri a m’Baibulo omatithandiza kukhazika bwino ukwati wathu ngati tiwatsatire. Chimodzi mwa zinthu zoyamba zimene Ambuye amatifunsa tikakwatirana, ndichokusiya abambo ndi amayi athu kuti tipange banja lathu, nyumba yathu yatsopano. Zoonadi, tiyenera kulemekeza makolo athu, koma zisankho zopangidwa tsopano ziyenera kukhala ndi mnzanu, banja lanu.
Ukwati uyenera kuperekedwa kwa Mulungu, aliyense ayenera kutenga udindo umene Mulungu wapereka mu mgwirizanowu, ndi kuika chikondi chanu m'manja mwa Mulungu, kulimbitsa chikondi chanu tsiku ndi tsiku ndi pemphero ndi mawu a Mulungu.
Ukwati ndi wa nthawi zonse, dongosolo limene Mulungu analipangira ukwati ndi la nthawi zonse, kusudzulana sikuli m'dongosolo lake, Mulungu amafuna kuti mukhale pamodzi mpaka imfa. Pali zinthu zoopsa monga kusakhulupirika kapena nkhanza, koma dongosolo loyambirira la Mulungu ndi lakuti mwamuna ndi mkazi akhale pamodzi mpaka imfa.
Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;
Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu.
Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake;
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.
koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; Koma inu simunaphunzira Khristu chotero, ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu; kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi. Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo mdierekezi. Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.
Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.
Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola, maso ako akunga a nkhunda. Taona, wakongolatu, bwenzi langa, mnyamatawe, inde, wakongoletsa; pogona pathu mpa msipu.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.
Nditawapitirira pang'ono, ndinampeza amene moyo wanga umkonda: Ndinamgwiriziza, osamfumbatula, mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai, ngakhale m'chipinda cha wondibala.
Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke nayo nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.
Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.
Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.
Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.
Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.
Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa. Ndinapita pa munda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona, ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.
Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake: Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.
Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.
Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.
Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.
koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Taona, wakongolatu, bwenzi langa, mnyamatawe, inde, wakongoletsa; pogona pathu mpa msipu.
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.
Zinthu zitatu zindithetsa nzeru, ngakhale zinai, sindizidziwa: Njira ya mphungu m'mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakati pa nyanja, njira ya mwamuna ndi namwali.
Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.
Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, Ana akazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo.
Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.
Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.
Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi; walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.
Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;
Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.
Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwake; pakuti chikondi chako chiposa vinyo.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.
Ndine wake wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine; aweta zake pakati pa akakombo.
Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,
Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana akazi inu a ku Yerusalemu.
Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.
Kudonthadontha tsiku lamvula, ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi. Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo; dzanja lake lamanja lingogwira mafuta.
Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi! Kodi chikondi chako sichiposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu!
Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu.