Mnzanga, chinthu chimodzi chomwe uyenera kumvetsa ndi kuvomereza ndichakuti nthawi ya Mulungu ndi yangwiro, ndipo zonse zomwe wamufunsa Mulungu zidzachitika mu nthawi yake.
Nthawi zambiri timayenda moyo wathu wodzaza ndi nkhawa chifukwa tikufuna zinthu zichitike mwachangu, koma Mulungu wanena momveka bwino m'mawu ake kuti chilichonse chili ndi nthawi yake, choncho pumula pang'ono ndipo upumule m'manja mwa Atate wako akumwamba.
Chilichonse chimafika nthawi yake yoyenera, pamalo ndi nthawi yoyenera. Tiyenera kumvetsa kuti nthawi yathu si nthawi ya Mulungu. Nthawi ya Mulungu imadziwika kuti *kairos*, kutanthauza nthawi yoyenera, nthawi yabwino, yoikidwa ndi yolondola. *Kairos* amatanthauza nthawi yokonzedwa kumwamba yomwe imawululiridwa padziko lapansi kutidalitsa.
Mulungu sadzafika mochedwa, khala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndipo yembekezera kuti chimene ukufuna chidzachitike. Mukapumula mwa Mulungu, mukuwonetsa chikhulupiriro chanu ndi chidaliro chomwe muli nacho m'mawu ake.
Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso; ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.
Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.
ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;
mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'Mwamba.
Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'chifuwa chanu m'ntchito zoipazo, koma tsopano anakuyanjanitsani m'thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake;
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.
Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo. Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.
Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;
Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.
Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.
Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,
Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;
Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera, amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu; kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.
koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.
Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.
pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu;
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.
Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu,
ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.
Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.
Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake.
Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.
m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha.
Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.
Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.
Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.
amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.
Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.
Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.
Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.
Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;
Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi, akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu; kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.
kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi, mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, nisizinalowa mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;