Mtima wanga ukufuna kuti mukachoke kuno, muzipita bwino pa zonse, ndipo mukhale ndi thanzi labwino, monga momwe mukupitira patsogolo mwauzimu. Ndikukhulupirira kuti Mulungu adzakudalitsani pa ulendo wanu.
Mau ambiri ochokera m'Baibulo angatilimbikitse, monga momwe lemba la 3 Yohane 1:2 limatiuza. Mulungu ali ndi malonjezo ambiri kwa ife, ndipo ndikukhulupirira kuti mudzapeza mphamvu ndi chiyembekezo mwa Iye pamene mukupitiriza ulendo wanu.
Zikomo kwambiri chifukwa chobwera, ndipo Mulungu akudalitseni.
Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.
Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu.
Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakulaka.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.
Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.
Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.
Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa.Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.
Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'ntchito zao.Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.
Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?
Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Ambuye.
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Lachiwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.
Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.
Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.
Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.
Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.
kuti kusakhale chisiyano m'thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.
Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Chikondi cha pa abale chikhalebe.Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.
mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.
Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.
Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.
Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana.Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea;kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;
Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka m'Masedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;pakuti m'Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.
Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu;ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
Mupatsane moni ndi chipsompsono cha chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.
ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;
ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a achifwamba?Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo.
Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.
Koma m'Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.
Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.
Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake,ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.