Ukwati ndi chinthu chapadera kwambiri, tsiku lodzala ndi malingaliro okongola, ndi nthawi yomwe umagwirizana ndi mnzanu kukhala thupi limodzi. Ndi chikondi ndi chiyembekezo, umatha kusangalala kwambiri ndi nthawi yosangalatsayi yodzala ndi chimwemwe ndi chiyamiko kwa Mulungu chifukwa chokuikira munthu uyu pambali pako.
Mulungu amaona ukwati wanu kukhala wofunika kwambiri, chifukwa si bwino kuchita chigololo kapena dama. Timapeza mavesi ambiri okhudza maudindo a mwamuna ndi mkazi, komanso momwe chikondi chimene mumalonjezana chiyenera kukhalira pa moyo wanu wonse.
Aliyense azilemekeza ukwati ndi kukhulupirirana, chifukwa Mulungu adzaweruza achigololo ndi onse ochita zonyansa. (Ahebri 13:4) Tiyenera kukumbukira kuti chikondi chiyenera kukhala champhamvu, kuti chizitha kupirira nthawi iliyonse yovuta, koposa zonse muyenera kukhala ndi Mulungu nthawi zonse kuti akuthandizeni ndi kukupatsani chipambano pa chilichonse, chikondi sichiyenera kukhala cha dyera, sichiyenera kufunafuna zake zokha, sichimadzikuza, sichimatha.
Muzigwirizana wina ndi mnzake, chifukwa cholemekeza Khristu. Akazi, muzigonjera amuna anu monga momwe mumagonjerera Ambuye. (Aefeso 5:21-22)
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake;kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;
Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke nayo nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.
Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha m'khosi zitatu sichiduka msanga.
Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.
Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.
Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.
Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.
Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake;
Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye,ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko. Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;
Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.
Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.
Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.
Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako;motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.
koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala;koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse.Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.
Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.
Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.
pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.
Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo;koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu.
Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.
Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale.Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu.Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe.
Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.
Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye chilekaniro:koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi; walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.