Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


150 Mau a Mulungu Ponseponse

150 Mau a Mulungu Ponseponse


Yeremiya 23:23-24

Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patali? Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:3

Maso a Yehova ali ponseponse, nayang'anira oipa ndi abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:27-28

kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:1-2

Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:15

Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:13-14

Yehova apenyerera m'mwamba; aona ana onse a anthu. M'malo akhalamo Iye, amapenya pansi pa onse akukhala m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:5

Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunaika dzanja lanu pa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:23

Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:39

Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi pa dziko lapansi; palibe wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 33:14

Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:3

Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 34:21

Pakuti maso ake ali pa njira ya munthu aliyense, napenya moponda mwake monse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:8

Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:14

Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:4-6

Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba. Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:11-12

Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:27

Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m'Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:6

Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:4

Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:13

Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:10

Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 6:3

Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 102:27

Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:13

Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:9

Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:8

Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:18

Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:48-49

Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena, Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:9

Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:15

Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 2:10-11

Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova. Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:1

Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:6

Kudziwa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:24

Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 6:18

Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu pa dziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:24

Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:20

Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:12

Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:16

Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:23-24

Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:22

Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:1

Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:17

Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:21

ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:151

Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:8

Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 16:17

Pakuti maso anga ali pa njira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:9

Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva? Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 11:7-9

Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna? Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika? Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji? Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji? Muyeso wake utalikira utali wake wa dziko lapansi, chitando chake chiposa cha nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:28

Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:7-8

Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso. Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:23

amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 31:8

Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:5-6

Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'chuuno, ngakhale sunandidziwa; kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 2:6

Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:17-18

Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:6-9

Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa. Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:7

Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:12

Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:3

Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:4

Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:36

Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13

Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:3-4

Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:4-5

Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake; chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake. Nyanja ndi yake, anailenga; ndipo manja ake anaumba dziko louma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:16

Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:6

Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:8

Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Yehova wa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:16

Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 12:10

M'dzanja mwake muli mpweya wa zamoyo zonse, ndi mzimu wa munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:3

ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:10

kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:6-7

Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:19

Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:5

Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:8

Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:17

Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:27

Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova; usanthula m'kati monse mwa mimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:1-2

Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha. Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu. Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa? Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao. Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu. Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu; amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi. Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:31-32

Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:2

Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:30

komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:10

Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:17

kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:21

ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 3:14

Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:10

Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi, kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 24:7

Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova, nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:7

Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:15

Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:14-15

Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine, monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 12:3

Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:13

pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:11-12

Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime pa phiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho. Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:9

Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:26

Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:5-6

Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja. Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 6:16-17

Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo. Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:6

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:33

Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:18

Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:6-7

Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu. Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:1-2

Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu. Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake. Ndipo Elikana ananka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo. Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova. Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake; nachipisa m'chimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko. Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi. Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda. Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova. Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta. Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka. Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:28

Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 14:19-20

Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao; Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja. nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzake usiku wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:5-6

Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:29-31

Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao. Ndipo m'mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. Ndipo kunali m'mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo. Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:23

Koma ndikhala ndi Inu chikhalire, mwandigwira dzanja langa la manja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:15

Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:14

Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:7

Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:2

Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:21-22

Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife m'ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo. Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:13-14

Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:5

Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:22-26

Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri! Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake? Kotero ngati simungathe ngakhale chaching'onong'ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:29

Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 7:22

Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 57:3

Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:12

Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 11:4

Yehova ali m'Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli m'Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 26:14

Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:18

Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 38:16-18

Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni? Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe? Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa? Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziwa chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:20

Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 61:4

Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 23:22

Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:24-25

Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja; satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 8:6

koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:16

Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa