Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


NDIME ZA CHIPULUMUTSO

NDIME ZA CHIPULUMUTSO

Ndikufuna ndikuuzeni nkhani yofunika kwambiri yokhudza chipulumutso. Chipulumutso chimabwera mukadzala ndi machimo anu, kenako mutadzala mumalandira Yesu mu mtima mwanu, ndipo mumasintha moyo wanu, musiya zinthu zonse zomwe Mulungu sakondwera nazo.

Chipulumutso kudzera mwa Yesu chimatipulumutsa ku mphamvu ya uchimo ndi imfa yauzimu. Mulungu amatiitana kuti tikhale ndi moyo woyera kuti tisunge mphatso ya chipulumutso, timasunga chipulumutso kudzera m'pemphero, Mawu a Mulungu ndi kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Khristu pamaso pa anthu.

Chipulumutso ndi mphatso yosapezeka, Mawu a Mulungu amanena kuti tili ochimwa, Khristu anafera aliyense wa ife. Chipulumutso tingochipeza kudzera mwa Ambuye wathu Yesukristu. (Machitidwe 4:12) Ndipo mulibe chipulumutso mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lopatsidwa kwa anthu, limene tingapulumutsidwe nalo.

Tiyeni tiyamikire mphatso ya chipulumutso cha moyo wosatha, tithokoze Mulungu potilola kupeza mphatsoyi ndipo tipemphe kuti atithandize kusunga mphatso yamtengo wapataliyi.




Yohane 3:3

Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:5

Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:9

kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:5-6

Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3

Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:15

Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:23

inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:26

Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:12-13

Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:6

Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:4-5

koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1-2

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:9-10

kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1-3

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:1

Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:7

Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:13

Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16

Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:1

Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:18

Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:14

Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:12

Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:44

Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:63

Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:4

Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:9

Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:13

amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:24

nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:11

amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:9

Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:22

Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:22-24

Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:4

mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili pa dziko lapansi m'chilakolako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:3

nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:38

Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:13-14

Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:29

Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1-2

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20

Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:22

amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16-17

Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:26-27

Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:10

Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:25

Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:11-14

Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse,ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:6

podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 8:10

Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13

amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa chikondi chake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:11

Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:2

Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:26

Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:14

koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:9

amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 20:31

koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:15

Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:5

Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:13

pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:36

Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:10

ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:24

amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:10

Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:7

Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:12

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:18-19

Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale.Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:40

Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:28

Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:14

Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:7

kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:16

Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:9

Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu, M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:17

ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:1

Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:5

Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:10

kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:14

koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:4

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kachisi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:25

amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:18

Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:24

Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:3

Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:36

Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4

Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:116

Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:2

Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:11

Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:19-22

Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:11

Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:3

Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:21

Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chipatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:19

Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:13

Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10-11

Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:50

Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:6

Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:16

Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:6

Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:1-2

Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:1

Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:137

Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:35

pakuti wondipeza ine apeza moyo; Yehova adzamkomera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:5

tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-2

Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.Mbeu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:25

kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:27

Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:12-14

ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa chikondi chake;amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wachilungamo ndi wokhulupirika, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu! Ambuye Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha nsembe yanu pa mtanda, chifukwa cholandira malo anga ndi kulipira mtengo umene ine sindingathe kulipira. Zikomo potsegula njira yatsopano yotchedwa chipulumutso kwa anthu onse. Zikomo Yesu wanga, chifukwa ndinu chitsanzo chachikulu cha chikondi ndi ubale wabwino pakati pa Mulungu ndi anthu. Mawu anu amati: "Tsono popeza talungamitsidwa ndi chikhulupiriro, tili naye mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu." Ndikukukondani Yesu, mwandiwombola, mwandipulumutsa ndi kundikhululukira, zikomo polipira ngongole yomwe ine sindingathe kulipira. Zikomo Yesu, mwandimasula ndi kundipulumutsa ndipo tsopano ndili mfulu ku chiweruzo chilichonse. Yesu wanga wabwino, ndikukuthokozani chifukwa chondikondera kotero kuti lero nditha kulengeza kuti mulimonse mmene zinthu zilili, Inu ndinu yankho. Nsembe yanu pa mtanda sinali yachabe, kudzera mmenemo ndapeza moyo umene ndimaufuna, ndapeza chikhululukiro, machiritso ndipo mwandibwezeretsa kwa Atate. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa