Mulungu ndiye mlengi wako, mtetezi wako, wosamalira wako. Ndi wamphamvuzonse, wachifundo, wokhululuka, wabwino. Tingadziwe Mulungu kudzera m'mawu ake. Amakuikira mtima ndipo wakupangira dongosolo labwino pa moyo wako.
Amadziwa zonse zisanachitike. Ndi chikondi chosatha. Pakuti Ine Yehova ndine Mulungu wako, wakugwira dzanja lako lamanja, nanena ndi iwe, Usawopa; Ine ndikuthandiza. (Yesaya 41:13)
Choncho Mulungu nthawi zonse adzakhala nafe, timangofunika kumuyandikila. Iye ndiye mlengi ndi wosamalira zinthu zonse, amene anapulumutsa dziko kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.
Ndipo ndidzayesa mudzi uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.
Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.
Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.
Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.
Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi.
Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.
Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.
Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.
Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.
Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.
Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.
Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, ang'ono ndi akulu.
Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.
Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.
Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.
pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.
pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;
Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.
Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.
Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.
Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.
Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.
Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu.
Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu.
Sindinapatukana nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa.
Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga.
Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.
Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.
Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.
Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.
Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu.
Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.
Imbirani Mulungu, imbirani; imbirani mfumu yathu, imbirani.
Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani ndi chilangizo.
Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake.
Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu,
ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Adzawapereka kumphamvu ya lupanga; iwo adzakhala gawo la ankhandwe.
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.
Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.
Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.
Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira, ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.
Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda.
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.
amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.