Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


64 Mau a Mulungu Olimbitsa Achinyamata

64 Mau a Mulungu Olimbitsa Achinyamata

Unyamata ndi nthawi yofunika kwambiri pa moyo wathu. Popanda mfundo zolimba, makhalidwe abwino, ndi kudziwa bwino Khristu, tingasochere m’dziko lodzala ndi mayesero. Ndikofunika kwambiri kumufunafuna Mulungu tili aang’ono, chifukwa nthawi zovuta ndi mayesero zikafika, ndi Iye yekha amene angatithandize kupambana.

Mulungu akufuna achinyamata omudziwa, omukhulupirira, ndi okhala moyo wom’kondweretsa. Achinyamata omwe amagwiritsitsa mawu ake ndi kutsatira malamulo ake. Tikatero, tidzakhala ndi moyo wodalitsidwa, ndipo ngakhale mavuto atafika, dzanja la Mulungu lidzatilimbitsa ndipo tidzakhalabe olimba m’chikhulupiriro chathu.

Kwa inu omwe mukuwerenga mawu awa, kumbukirani kuti Khristu akubwera posachedwa. Mufunafuneni tsopano popeza mungamupeze, musanachedwe. Ndi chikondi cha Yesu chomwe chingakuthandizeni kupirira mpaka kumapeto, chifukwa ali ndi mapulani abwino kwa inu, ndipo nthawi yomufunafuna ndi lero!

Kumbukiraninso kuti Mulungu ali nanu pakati pa mavuto ndi mayesero omwe mukukumana nawo. Khalani olimba mtima ndipo thawirani kwa Atate wanu wakumwamba, Iye adzakupatsani chipambano.




2 Timoteyo 2:22

Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12

Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:1-2

Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo; Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona. Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba. Pamodzi ndi izi, mwananga, tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi. Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa. ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:13

Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:21-22

Yesani zonse; sungani chokomacho, Mupewe maonekedwe onse a choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:12

Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:23

Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:16

popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:10

Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga, koma Yehova anditola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:9

Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18

Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:26

Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:17

Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:41

Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:10

Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:3

pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-4

Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko. Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:16

Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 3:4

Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 23:10-11

Koma adziwa njira ndilowayi; atandiyesa ndidzatuluka ngati golide. Phazi langa lagwiratu moponda Iye, ndasunga njira yake, wosapatukamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1-3

Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 8:10

Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:9

Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:10

Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:13-14

Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani. Zanu zonse zichitike m'chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:1-2

Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha. Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu. Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa? Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao. Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu. Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu; amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi. Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:9

Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:9

koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wamuyaya, wamkulu, komanso wamphamvu ndinu! Ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, ndikupempherera achinyamata onse omwe akukumana ndi mayesero. Mzimu Wanu Woyera uwalimbikitse ndi kuwatsogolera nthawi zonse. Ambuye, apatseni nzeru zosiyanitsa chabwino ndi choipa, kuti asanyengedwe, koma akhale okonzeka ndi odziteteza ku ziwembu zonse za mdani. Pakuti kwalembedwa, "Khalani oyera, chifukwa Ine ndine woyera." Ambuye, awathandize kuzindikira mayesero onse a mdani, awateteze ku anthu olankhula monyenga ndi okopa. Awathandize kusankha zoyenera ndi kupambana pa mayesero onse. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa