Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.
Numeri 6:25 - Buku Lopatulika Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo; |
Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.
Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.
Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo; mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu, ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
Ndipo Iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo.
Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pamalo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye.
Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.