Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Yosefe ataona Benjamini, mng'ono wake weniweni uja, adati “Uyu ayenera kukhala mng'ono wanu wotsiriza uja munkandiwuzayu. Mulungu akudalitse, mwana wanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Pomwazamwaza maso Yosefe anaona Benjamini, mʼbale wake weniweni wa bere limodzi, ndipo anafunsa, “Kodi uyu ndiye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri amene munkandiwuza uja?” Kenaka anati, “Ambuye akukomere mtima mwana wanga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:29
22 Mawu Ofanana  

ana aamuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini;


Tonse tili ana aamuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda.


Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.


Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.


Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito.


Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.


Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.


Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.


Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake;


Pakuti anthu adzakhala mu Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha.


Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto.


Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.


Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;


Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.


Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!


kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


Chikondi cha pa abale chikhalebe.


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa