Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 86:16 - Buku Lopatulika

16 Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo; mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu, ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo; mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu, ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mundiyang'ane ndipo mundichitire chifundo. Mundipatse mphamvu zanu ine mtumiki wanu, mundipulumutse ine mwana wa mdzakazi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo; perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 86:16
18 Mawu Ofanana  

Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga.


Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo, monga mumatero nao akukonda dzina lanu.


Ine ndine wanu, ndipulumutseni pakuti ndinafuna malangizo anu.


Tsiku loitana ine, munandiyankha, munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.


Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo; pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika.


Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?


Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.


Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu; mumtima mwake muli makwalala a ku Ziyoni.


Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.


Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.


kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa