Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliyasibu ndi Eliyasibu anabala Yoyada,
Nehemiya 3:1 - Buku Lopatulika Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga chipata chankhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka nsanja ya Hananele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Eliyasibu, mkulu wa ansembe, adayamba kugwira ntchito pamodzi ndi ansembe anzake, ndipo adamanga Chipata cha Nkhosa. Adachipatulira Mulungu naika zitseko zake. Khoma limene adapatulalo lidafika ku Nsanja ya Zana, mpakanso ku Nsanja ya Hananele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli. |
Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliyasibu ndi Eliyasibu anabala Yoyada,
ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.
Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.
Chinkana ichi, Eliyasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anachita chibale ndi Tobiya,
Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe.
Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu.
Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda.
Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata);
Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;
Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.
Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.
Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.
Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.