Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 12:39 - Buku Lopatulika

39 ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata Chansomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka kuchipata chankhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Tidadzeranso pa Chipata cha Efuremu, pa Chipata Chakale, pa Chipata cha Nsomba, pa Nsanja ya Hananele, pa Nsanja ya Zana, mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo potsiriza tidakaima ku Chipata cha Mlonda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Tinadutsanso Chipata cha Efereimu, Chipata cha Yesana, Chipata cha Nsomba, Nsanja ya Hananeli, Nsanja ya Zana mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo mdipiti uwu unakayima pa Chipata cha Mlonda.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:39
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.


Atatero, magulu awiriwo a iwo oyamikira anaima m'nyumba ya Mulungu, ndipo ine ndi limodzi la magawo awiri a olamulira pamodzi ndi ine;


Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.


Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.


Ndi Chipata cha Nsomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.


Ndi Chipata Chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.


Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la Chipata cha Efuremu.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.


Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.


Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku Chipata cha Nsomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.


Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa