Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 13:28 - Buku Lopatulika

28 Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe uja, anali atakwatira mwana wa Sanibalati wa ku Horoni. Nchifukwa chake ndidampirikitsa kuti achoke ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:28
14 Mawu Ofanana  

ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende.


Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliyasibu ndi Eliyasibu anabala Yoyada,


M'masiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani, ndi Yaduwa, Alevi analembedwa akulu a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariusi wa ku Persiya.


Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi.


Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.


Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?


Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.


Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukulu, naseka Ayuda pwepwete.


Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.


Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu, niyendetsapo njinga ya galeta.


Mfumu yokhala pa mpando woweruzira ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa