Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 5:2 - Buku Lopatulika

2 Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Koma pali thamanda m'Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa m'Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Kumeneko kuli dziŵe, dzina lake pa Chiyuda ndi Betesida. Dziŵeli lili pafupi ndi Chipata cha Nkhosa, ndipo nlozingidwa ndi makonde asanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 5:2
14 Mawu Ofanana  

ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.


Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.


Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda.


Inu munapanganso chosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anachichita icho, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.


Ndipo inu munaona kuti pa mzinda wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.


Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma mu Chihebri, Gabata.


ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa mu Chihebri, Gologota:


Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mzindawo; ndipo linalembedwa mu Chihebri, ndi mu Chilatini, ndi mu Chigriki.


Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye mu Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.


M'menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.


Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse.


Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:


Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa mu Chihebri Armagedoni.


Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa