Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 5:3 - Buku Lopatulika

3 M'menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 M'menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 M'makondemo munkagona anthu ambiri odwala, akhungu, opunduka miyendo ndi opuwala ziwalo. [Iwoŵa ankadikira kuti madzi agwedezeke.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 5:3
12 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.


Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;


Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.


Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.


Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa;


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.


Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.


Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa