Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 12:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Tsono ansembe ndi Alevi adachita mwambo wa kudziyeretsa. Mwambowu adachitiranso anthu, ndiponso zipata ndi khoma la mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Tsono ansembe ndi Alevi anachita mwambo wodziyeretsa. Pambuyo pake anachita mwambo woyeretsa anthu onse ndi khoma la Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:30
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:


Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele.


Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha ntchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula.


nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kuchotsa zoipsa m'malo opatulika.


Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza,


ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake;


Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.


Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:


ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa