Nehemiya 12:31 - Buku Lopatulika31 Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201431 Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa31 Ineyo ndidadza nawo akuluakulu a ku dziko la Yuda ndipo ndidakwera nawo pa khoma. Ndidasankha magulu aŵiri mwa iwo, kuti aziyenda mu mdipiti ndi kumathokoza Mulungu. Mdipiti wina unkadzera cha ku dzanja lamanja pa khoma mpaka kukafika ku Chipata cha Kudzala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero31 Ine ndinabwera nawo atsogoleri a dziko la Yuda ndi kukwera nawo pa khoma. Ndipo ndinasankha magulu awiri akuluakulu oyimba nyimbo za matamando. Gulu limodzi linadzera mbali ya ku dzanja lamanja pa khoma mpaka ku Chipata cha Kudzala. Onani mutuwo |
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.