Nehemiya 6:1 - Buku Lopatulika1 Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata); Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata); Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Kudangotero kuti Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndiponso adani athu ena adamva kuti tidatha kumanganso khoma, ndipo kuti sipadatsale mpamodzi pomwe pogumuka, ngakhale tinali tisanaike zitseko pa zipata. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Pamenepo Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndi adani athu anamva kuti ndatsiriza ntchito yomanganso khoma ndi kuti palibe mpata umene watsala ngakhale kuti pa nthawi imeneyi ndinali ndisanayike zitseko pa zipata. Onani mutuwo |