Nehemiya 2:20 - Buku Lopatulika20 Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeretsa; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, mu Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, m'Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Ine ndidaŵayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino, ndipo ife atumiki ake tiyambapo kumanga. Koma inuyo mulibe chanu muno, mulibe mphamvu yolandirira malo muno, ndipo mulibenso chilichonse chokumbutsa za inu mu Yerusalemu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.” Onani mutuwo |
Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.