Nehemiya 3:1 - Buku Lopatulika1 Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga chipata chankhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka nsanja ya Hananele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake Eliyasibu, mkulu wa ansembe, adayamba kugwira ntchito pamodzi ndi ansembe anzake, ndipo adamanga Chipata cha Nkhosa. Adachipatulira Mulungu naika zitseko zake. Khoma limene adapatulalo lidafika ku Nsanja ya Zana, mpakanso ku Nsanja ya Hananele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli. Onani mutuwo |
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.