Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:32 - Buku Lopatulika

32 Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi chipata chankhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa, amisiri a golide ndi anthu amalonda adakonza chigawo chao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza ndi amisiri a golide ndi anthu amalonda.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:32
5 Mawu Ofanana  

ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.


Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.


Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya antchito a m'kachisi, ndi ya ochita malonda, pandunji pa Chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya.


Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lachitando.


Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa