Nehemiya 3:31 - Buku Lopatulika31 Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya antchito a m'kachisi, ndi ya ochita malonda, pandunji pa Chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201431 Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya Anetini, ndi ya ochita malonda, pandunji pa chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa31 Pambali pa iyeyo Malikiya, mmodzi mwa amisiri a golide, adakonza chigawo china mpaka kukafika ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda. Chigawo chimenechi chidaayang'anana ndi Chipata cha Mifikada, kufikira ku chipinda chapamwamba chapangodya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero31 Motsatana naye, Malikiya mmodzi mwa amisiri a golide anakonza chigawo china mpaka ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda moyangʼanana ndi chipata cha Mifikade ndiponso mpaka pa chipinda chapamwamba chapangodya. Onani mutuwo |