Masalimo 92:4 - Buku Lopatulika Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu. |
Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.
Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye; ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.
Pakuti Yehova atero, Imbirani Yakobo ndi kukondwa, fuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israele.
Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.
Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.