Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.
Masalimo 83:2 - Buku Lopatulika Pakuti taonani, adani anu apokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti taonani, adani anu aphokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onani, adani anu akuchita chiwawa. Amene adana nanu akukuukirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo. |
Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.
Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu; kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka.
Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu; aika mbendera zao zikhale zizindikiro.
Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!
Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.
Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.
Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.
Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.
Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule.
Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.
Ndipo mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa mu Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.
Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.
Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.
Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.