Machitidwe a Atumwi 17:5 - Buku Lopatulika5 Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Koma Ayuda ena adachita nsanje, choncho adasonkhanitsa anthu opandapake ongoyendayenda, nayambitsa chipolowe mumzindamo. Adathamangira ku nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Silasi kuti aŵatulutsire ku anthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Koma Ayuda ena anachita nsanje; kotero anasonkhanitsa anthu akhalidwe loyipa ochokera pa msika ndipo napanga gulu nayambitsa chipolowe mu mzindawo. Anathamangira ku nyumba ya Yasoni kukafuna Paulo ndi Sila kuti awabweretse pa gulu la anthu. Onani mutuwo |