Machitidwe a Atumwi 21:30 - Buku Lopatulika30 Ndipo mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa mu Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201430 Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa m'Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa30 Tsono mumzinda monse mudaloŵa chisokonezo ndipo anthu onse adathamangira pamodzi namgwira Pauloyo. Adamkokera kunja kwa Nyumba ya Mulungu, nkutseka pa makomo nthaŵi yomweyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero30 Mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anabwera akuthamanga kuchokera kumbali zonse. Anamugwira Paulo, namukokera kunja kwa Nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo anatseka zipata. Onani mutuwo |