Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 23:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Anthu aja adafika pokangana koopsa, kotero kuti mkulu wa asilikali uja ankaopa kuti angamkadzule Paulo. Choncho adalamula asilikali kuti, “Pitani mukamlanditse kwa anthuwo, mukamloŵetse m'linga la asilikali.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mkangano unakula kwambiri kotero kuti mkulu wa asilikali anachita mantha kuti mwina anthu angakhadzule Paulo. Iye analamulira asilikali ake apite kukamuchotsa pakati pawo mwamphamvu ndi kubwera naye ku malo a asilikaliwo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 23:10
16 Mawu Ofanana  

Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.


Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?


kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.


Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.


Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.


Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa chakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye kubwalo lao la akulu a milandu.


Koma m'mawa mwake anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga;


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.


Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa