Mateyu 27:24 - Buku Lopatulika24 Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Pilato adaona kuti sakuphulapo kanthu, ndipo kuti anthu ali pafupi kuchita chipwirikiti. Choncho adaitanitsa madzi, nkusamba m'manja pamaso pa anthu onse, nanena kuti, “Ine ndiye ndilibe kanthu pa imfa ya munthuyu. Izo nzanu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Pilato ataona kuti samaphulapo kanthu, koma mʼmalo mwake chiwawa chimayambika, anatenga madzi nasamba mʼmanja mwake pamaso pa gulu la anthu. Iye anati “Ine ndilibe chifukwa ndi magazi a munthu uyu, ndipo uwu ndi udindo wanu!” Onani mutuwo |