Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 81:15 - Buku Lopatulika

15 Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga, koma nyengo yao ikadakhala yosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga, koma nyengo yao ikadakhala yosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 “Anthu amene amadana ndi Chauta, akadakhwinyata pamaso pake, ndipo tsoka lao likadakhala mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 81:15
13 Mawu Ofanana  

Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.


Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.


Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo.


Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita;


Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga.


akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,


Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.


Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa