Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 81:14 - Buku Lopatulika

14 Ndikadagonjetsa adani ao msanga, ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndikadagonjetsa adani ao msanga, ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 bwenzi posachedwa nditagonjetsa adani ao, ndipo dzanja langa likadakantha amaliwongo ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 81:14
9 Mawu Ofanana  

Atigonjetsera anthu, naika amitundu pansi pa mapazi athu.


Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;


ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.


Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.


Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,


dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa