Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mpaka apa anthu aja ankamvetsera bwinobwino mau a Paulo. Koma pamene adadzatchula mau otsirizaŵa, iwo adayamba kufuula kuti, “Munthu wotere koma kungokonzeratu. Sayeneranso kukhala moyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:22
6 Mawu Ofanana  

Koma iwo onse pamodzi anafuula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Barabasi;


Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.


pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye.


Ndipo Fesito anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.


natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa