Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 3:8 - Buku Lopatulika

Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mumatipulumutsa ndinu, Inu Chauta. Madalitso anu akhale pa anthu anu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. Sela

Onani mutuwo



Masalimo 3:8
22 Mawu Ofanana  

Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu.


Ine ndine wanu, ndipulumutseni pakuti ndinafuna malangizo anu.


Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu, Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.


Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu, mundipulumutse ndi chifundo chanu.


Apitetu ngati madzi oyenda; popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.


Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Muwachititse mantha, Yehova; adziwe amitundu kuti ali anthu.


Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.


Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.


Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.


Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.


Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.


Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.


Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.


Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.


osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.


Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;


ndipo afuula ndi mau aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.