Masalimo 3:2 - Buku Lopatulika Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ambiri akamalankhula za ine amati, “Mulungu samupulumutsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela |
Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.
Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.
Munapombosola uta wanu; malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona. Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.