Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 3:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu ambiri akamalankhula za ine amati, “Mulungu samupulumutsa.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 3:2
14 Mawu Ofanana  

akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo,


Onse amene amandiona amandiseka; amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti


Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela


Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. Sela


Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? Sela.


Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. Sela


Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo pamene adani anga akundinyoza, tsiku lonse akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?”


Misozi yanga yakhala chakudya changa usana ndi usiku, pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?”


Iwo amati, “Mulungu wamusiya; mutsatireni ndi kumugwira, pakuti palibe amene adzamupulumutse.”


Munapita kukalanditsa anthu anu, kukapulumutsa wodzozedwa wanu. Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa, munawononga anthu ake onse. Sela


Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani. Sela Ulemerero wake unaphimba mlengalenga ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.


Munasolola uta wanu mʼchimake, munayitanitsa mivi yambiri. Sela Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa