Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Masalimo 16:8 - Buku Lopatulika Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. |
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.
Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.