Masalimo 110 - Buku LopatulikaUfumu wa Ambuye Salimo la Davide. 1 Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. 2 Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; chitani ufumu pakati pa adani anu. 3 Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu. 4 Yehova walumbira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki. 5 Ambuye padzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. 6 Adzaweruza mwa amitundu, adzadzaza dziko ndi mitembo; adzaphwanya mitu m'maiko ambiri. 7 Adzamwa kumtsinje wa panjira; chifukwa chake adzaweramutsa mutu wake. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi