Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Masalimo 135:3 - Buku Lopatulika Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta, pakuti ngwabwino. Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nlokoma kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino; imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero, |
Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.