Masalimo 135:1 - Buku Lopatulika Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova! Lemekezani inu atumiki a Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova! Lemekezani inu atumiki a Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta. Tamandani dzina la Chauta, Perekani matamando, inu atumiki a Chauta, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova. Tamandani dzina la Yehova; mutamandeni, inu atumiki a Yehova, |
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.
Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.