Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.
Masalimo 12:1 - Buku Lopatulika Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Thandizeni, Inu Chauta, palibenso munthu wosamala za Inu, okhulupirika sapezekanso pakati pa anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu. |
Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.
ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi Azaziya, ndi azeze akuimbira mwa Seminiti, kutsogolera maimbidwe.
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.
Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.
Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza.
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.
Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.
Koma m'mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!
Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.