Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 6:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mulungu atayang'ana dziko lapansi, adaona kuti ndi lonyansa, chifukwa anthu onse anali oipa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mulungu atayangʼana, anaona kuti dziko layipadi chifukwa cha makhalidwe oyipa a anthu onse pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 6:12
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu,


ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.


Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.


Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.


Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.


Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi, ndi anthu onse:


Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;


Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.


Maso a Yehova ali ponseponse, nayang'anira oipa ndi abwino.


ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.


ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa