Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 14:30 - Buku Lopatulika

30 Koma m'mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Koma m'mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Koma ataona m'mene ikuwombera mphepo, adachita mantha, nkuyamba kumira. Tsono adafuula kuti, “Ambuye, pulumutseni!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 14:30
17 Mawu Ofanana  

Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mzinda ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji?


Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.


Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?


Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa