Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 14:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Yesu adati, “Chabwino, bwera.” Tsono Petro adatuluka m'chombo nayamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Iye anati, “Bwera.” Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 14:29
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa Inu pamadzi.


Koma m'mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.


Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.


Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.


Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadire thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa