Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeretsa kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
Luka 7:16 - Buku Lopatulika Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onse adachita mantha, nayamba kutamanda Mulungu. Adati, “Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu.” Adatinso, “Mulungu wadzathandiza anthu ake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.” |
Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeretsa kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.
Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.
kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.
Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake.
Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko lonse la mapiri a Yudeya.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikire nyengo ya mayang'aniridwe ako.
Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.
Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;
Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.
Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.
Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera.
Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.
Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?
Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.
Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.
Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.
Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.
Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;